Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 12

Mawu Oyamba a Cigawo 12

Yesu anali kuphunzitsa anthu za Ufumu wa kumwamba. Anaŵaphunzitsanso kuti azipemphela kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe, Ufumu wake ubwele, komanso kuti cifunilo cake cicitike pa dziko lapansi. Ngati ndimwe kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa kuti pemphelo imeneyi ni yofunika kwambili kwa ise. Yesu sanalole kuti Satana amutaitse cikhulupililo cake mwa Mulungu. Yesu anasankha atumwi ake, oyamba kusankhidwa kuti akalamulile mu Ufumu wa Mulungu. M’cigawo cino, mudzaona kuti Yesu anali wodzipeleka pa kulambila koona. Cinanso, Yesu anali kukonda kuthandiza anthu. N’cifukwa cake anacilitsa odwala, kudyetsa anjala, ngakhalenso kuukitsa akufa. Mwa izi, Yesu anaonetsa zimene Ufumu wa Mulungu udzacitila anthu.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 74

Pamene Yesu Anakhala Mesiya

Kodi Yohane atanthauza ciani pokamba kuti Yesu ni Mwanawankhosa wa Mulungu?

PHUNZILO 75

Mdyelekezi Ayesa Yesu

Katatu konse Mdyelekezi ayesa Yesu. Kodi ni mayeselo atatu ati amene ayesedwa nawo? Nanga Yesu ayankha bwanji?

PHUNZILO 76

Yesu Ayeletsa Kacisi

N’cifukwa ciani Yesu akuthamangitsa nyama m’kacisi, na kugubuduza mathebulo a osintha ndalama?

PHUNZILO 77

Mzimayi Akumana na Yesu pa Citsime

Mzimayi wacisamariya adabwa kuona kuti Yesu akukamba naye. Cifukwa? Kodi Yesu amuuza ciani mzimayiyo cimene sauzepo munthu aliyense?

PHUNZILO 78

Yesu Analalikila Uthenga wa Ufumu

Yesu auza ophunzila ake kukhala “asodzi a anthu.” M’kupita kwa nthawi, Yesu aphunzitsa anthu 70 nchito yolalikila uthenga wabwino.

PHUNZILO 79

Yesu Acita Zozizwitsa Zambili

Kulikonse kumene wayenda, anthu odwala abwela kwa iye kuti awacilitse, ndipo awacilitsadi. Iye aukitsa ngakhale kamtsikana kamene kamwalila.

PHUNZILO 80

Yesu Asankha Atumwi 12

Kodi Yesu wasankha atumwi 12 kuti agwile nchito yanji? Kodi ungakumbukile maina awo?

PHUNZILO 81

Ulaliki wa pa Phili

Yesu aphunzitsa mfundo zofunika kwambili ku khamu la anthu limene lasonkhana.

PHUNZILO 82

Yesu Anaphunzitsa Otsatila Ake Kupemphela

Kodi ni zinthu zotani zimene auza otsatila ake kupitiliza kupempha?

PHUNZILO 83

Yesu Anadyetsa Khamu la Anthu

Kodi cozizwitsa ici citiphunzitsa ciani za Yesu na Yehova?

PHUNZILO 84

Yesu Anayenda pa Madzi

Kodi uganiza kuti atumwi amvela bwanji pamene akuona cozizwitsa cimeneci?

PHUNZILO 85

Yesu Acilitsa pa Sabata

N’cifukwa ciani ena sanakondwele na zimene Yesu acita?

PHUNZILO 86

Yesu Aukitsa Lazaro

Pamene Yesu aona Mariya akulila, nayenso ayamba kulila. Koma mwamsanga cisoni cawo cisintha kukhala cimwemwe.