Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Oyamba a Cigawo 14

Mawu Oyamba a Cigawo 14

Akhristu oyambilila analalikila uthenga wabwino wa Ufumu mpaka ku madela akutali kwambili pa dziko. Yesu anaŵauza kumene anafunika kukalalikila. Ndipo mozizwitsa anathandiza ophunzila ake kuphunzitsa anthu mu vitundu vawo. Yehova anawalimbitsa mtima kuti apilile pokumana na mazunzo oopsa.

Yesu anapatsa mtumwi Yohane masomphenya oona ulemelelo wa Yehova. M’masomphenya ena, Yohane anaona Ufumu wa kumwamba ukugonjetsa Satana na kuthetsa ulamulilo wake kwamuyaya. Yohane anaona Yesu akulamulila monga Mfumu pamodzi ndi anthu 144,000. Yohane anaona dziko lonse likusintha kukhala paradaiso, mmene aliyense anali kulambila Yehova mwamtendele, komanso mogwilizana.

M'CIGAWO CINO

PHUNZILO 94

Ophunzila a Yesu Alandila Mzimu Woyela

Kodi mzimu woyela uŵapangitsa kucita zozizwitsa zotani?

PHUNZILO 95

Palibe Akanawaletsa Kulalikila

Atsogoleli acipembedzo amene anapha Yesu, lomba akuopseza atumwi kuti aleke kulalikila. Koma iwo alephela.

PHUNZILO 96

Yesu Asankha Saulo

Saulo ni mdani wankhanza wa Akhristu, koma zinthu zatsala pang’ono kusintha.

PHUNZILO 97

Koneliyo Alandila Mzimu Woyela

N’cifukwa ciani Mulungu watumiza Petulo kwa munthu uyu amene si Myuda?

PHUNZILO 98

Cikhristu Cifalikila Kumadela Akutali

Mtumwi Paulo pamodzi na amishonale anzake ayamba nchito yolalikila kumadela akutali.

PHUNZILO 99

Woyang’anila Ndende Aphunzila Coonadi

N’cifukwa ciani Paulo na Sila aponyedwa m’ndende? Nanga woyang’anila ndende aphunzila bwanji coonadi

PHUNZILO 100

Paulo na Timoteyo

Kwa zaka zambili, amuna aŵiliwa aseŵenzela pamodzi monga mabwenzi komanso atumiki a Mulungu.

PHUNZILO 101

Paulo Atumizidwa ku Roma

Pa ulendowu, akumana na zovuta zambili. Koma palibe vuto lililonse lingapangitse mtumwiyu kubwelela kumbuyo.

PHUNZILO 102

Masomphenya a Yohane

Yesu amuonetsa masomphenya osiyana-siyana a zakutsogolo.

PHUNZILO 103

“Ufumu Wanu Ubwele”

Masomphenya amene Yohane aona, akuonetsa mmene Ufumu wa Mulungu udzasinthila umoyo pa dziko lapansi.