Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 3

Ndinu Mphamvu Ndi Chiyembekezo Chathu Ndipo Timakudalirani

Ndinu Mphamvu Ndi Chiyembekezo Chathu Ndipo Timakudalirani

(Miyambo 14:26)

  1. 1. Yehova munatilonjeza

    Moyo wosathatu.

    Zimatilimbikitsadi.

    Timauza onse.

    Koma pena timada nkhawa

    Chifukwa cha mavuto.

    Chiyembekezo chathunso

    Chimatha kuchepa.

    (KOLASI)

    Mulungu inu ndinu

    Mphamvu yathu.

    Inde, mumatithandiza.

    Mwalimbitsa

    Chiyembekezo chathu.

    Timadalira inuyo.

  2. 2. Yehova muzitikumbutsa,

    Tisamaiwale

    Kuti mumatithandiza

    Tikamavutika.

    Tikakumbukira mfundoyi

    Timapezanso mphamvu

    Ndipo timalimba mtima

    Kutumikirabe.

    (KOLASI)

    Mulungu inu ndinu

    Mphamvu yathu.

    Inde, mumatithandiza.

    Mwalimbitsa

    Chiyembekezo chathu.

    Timadalira inuyo.