Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 3

Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

Ndimwe Mphamvu Zathu, Ciyembekezo, na Cidalilo Cathu

(Miyambo 14:26)

  1. 1. O Yehova, munalonjeza

    za moyo wosatha.

    Tifuna kuuza ena

    za lonjezo lanu.

    Mavuto amatifoketsa,

    Tisoŵa na cocita.

    Komanso timaiŵala

    za lonjezo lanu.

    (KOLASI)

    Ise timakudalilani,

    M’lungu.

    Kuti mudzatithandiza.

    Pamene tikulalikila anthu,

    tipeza mphamvu

    mwa imwe.

  2. 2. Tithandizeni kukumbuka

    kuti mutikonda.

    Ngakhale timavutika,

    Simumatisiya.

    Tilalikila mosaopa

    kwa amene tapeza.

    Mumatilimbitsa mtima

    Pophunzitsa anthu.

    (KOLASI)

    Ise timakudalilani,

    M’lungu.

    Kuti mudzatithandiza.

    Pamene tikulalikila anthu,

    tipeza mphamvu

    mwa imwe.

(Onaninso Sal. 72:13,14; Miy. 3:5, 6, 26; Yer. 17:7.)