Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 10

Tamandani Yehova Mulungu Wathu

Tamandani Yehova Mulungu Wathu

(Salimo 145:12)

  1. 1. Tamanda Yehova M’lungu.

    Phunzitsa za dzina lake.

    Chenjeza anthu adziwe

    Tsiku lake layandikira.

    Walamula kuti Mwana wake

    Akhale Mfumu padziko.

    Udziwitse mitundu ya anthu

    Kuti adzatidalitsa.

    (KOLASI)

    Tamanda Yehova M’lungu.

    Lengeza kuti ndi wamphamvu.

  2. 2. Tamanda Yehova M’lungu.

    Uimbe mosangalala.

    Sonyeza khama lakotu

    Polalikira anthu onse.

    Ngakhale Mulungu ndi wamphamvu,

    Iye amadzichepetsa.

    Ndi wachifundo chachikuludi,

    Amayankha mapemphero.

    (KOLASI)

    Tamanda Yehova M’lungu.

    Lengeza kuti ndi wamphamvu.