Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 12

Mulungu Wamkulu, Yehova

Mulungu Wamkulu, Yehova

(Ekisodo 34:6, 7)

  1. 1. M’lungu Wamkulu

    ndimwe Yehova,

    Atate wacikondi tidzakutamandani.

    Ndimwe wabwino mu zinthu zonse.

    Ndimwe M’lungu kosatha.

  2. 2. Atate wathu

    mumatikonda.

    Olo ndise ocimwa mumatisamalila.

    Tiyamikila mumatiyankha,

    Ise tikapemphela.

  3. 3. Mokweza mau za

    padzikoli

    Na zonse za kumwamba zimakuimbilani.

    Na mtima wonse tidzatamanda

    Imwe Yehova M’lungu.

(Onaninso Deut. 32:4; Miy. 16:12; Mat. 6:10; Chiv. 4:11.)