NYIMBO 13
Titsanzire Yesu
-
1. Yehova Mulungu
Anatikondadi,
Anapereka Yesu monga dipo.
Yesu analola
Kudzakhala munthu.
Anayeretsa dzina la M’lungu.
-
2. Yesu ankakonda
Mawu a Mulungu.
Ndi amene ankamupatsa nzeru.
Ankatumikira
Mokhulupirika
Ndipo anasangalatsa M’lungu.
-
3. Titsanzire
Yesu Potamanda M’lungu
Komanso muzochita zathu zonse.
Tizimutsanzira
M’moyo wathu wonse
Ndipo tizisangalatsa M’lungu.
(Onaninso Yoh. 8:29; Aef. 5:2; Afil. 2:5-7.)