NYIMBO 13
Khristu ni Citsanzo Cathu
(1 Petulo 2:21)
-
1. Timayamikila,
Cikondi ca M’lungu—
Anapeleka Yesu Mwana wake.
Khristu’a naonetsa,
Citsanzo cabwino—
Anayeletsa dzina Ia M’lungu.
-
2. Mau a Yehova,
Anamuthandiza,
Kuti akhale wokhulupilika.
Anatumikila
M’lungu mokondwela,
Tidzatengela citsanzo cake.
-
3. Khristu’a natipatsa
Citsanzo cabwino—
Anatamanda Yehova Atate.
Ise tilengeze
Ufumu wa M’lungu.
Tidzalandila moyo wosatha.
(Onaninso Yoh. 8:29; Aef. 5:2; Afil. 2:5-7)