Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 15

Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

(Aheberi 1:6)

  1. 1. Tamandani Yesu

    Mfumu yodzozedwayo,

    Yokonda choonadi 

    Komanso chilungamo. 

    Atavala ulemu 

    Ndi ulemerero, 

    Adzayeretsa dzina

    La Yehova M’lungu.

    (KOLASI)

    Tamandani Yesu 

    Wodzozedwa wa M’lungu.

    Wakhala pa Ziyoni 

    Mongadi Mfumu yathu.

  2. 2. Tamandani Yesu

    Yemwe anatifera. 

    Anapereka dipo, 

    Timakhululukidwa.

    Mkwatibwi wake pano 

    Akudikirira 

    Kuti alamulire 

    Limodzi ndi Yesu. 

    (KOLASI)

    Tamandani Yesu 

    Wodzozedwa wa M’lungu.

    Wakhala pa Ziyoni 

    Mongadi Mfumu yathu.