Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 20

Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

(1 Yohane 4:9)

  1. 1. Yehova tinali

    Opanda tsogolo,

    Komano dipo

    Lathandiza tonse.

    Tikudzipereka

    Kwa inu kosatha.

    Tiphunzitse anthu

    Akudziweninso.

    (KOLASI)

    Munaperekatu

    Mwana wanu yekha.

    Tidzakuimbirani,

    Za mphatsoyi mpaka kale.

  2. 2. Chikondi chanuchi

    Ndi chachikuludi

    Komanso mumatikomera

    Mtima.

    Yoposa zonsezi

    Ndi mphatso ya Yesu.

    Anatifera kuti

    Tipulumuke.

    (KOLASI)

    Munaperekatu 

    Mwana wanu yekha.

    Tidzakuimbirani,

    Za mphatsoyi mpaka kale.

    (KUMALIZA)

    Yehova, Atate, zikomo kwambiri.

    Tidzakumbukira mphatsoyi mpaka kale.

(Onaninso Yoh. 3:​16; 15:13.)