Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 24

Bwerani Kuphiri la Yehova

Bwerani Kuphiri la Yehova

(Yesaya 2:​2-4)

  1. 1. Phiri la Yehova

    Tangoliyang’anani.

    Lakwezedwa pamwamba

    Pa mapiri onse.

    Anthu akubwera

    Kuchokera kutali.

    Akuitanizana

    Bwerani kwa M’lungu.

    Tsopano wochepa

    Wasanduka mtundu wamphamvu.

    Tikuona kuti

    Tikudalitsidwa ndi M’lungu.

    Ambiri tsopano

    Akuvomerezadi

    Ulamuliro wake

    Mokhulupirika.

  2. 2. Yesu walamula

    Kuti tipite konse

    Tikalalikire

    Uthenga wa Ufumu.

    Khristu wayambano

    Ulamuliro wake

    Ndipo akuti tikhale

    Kumbali yake.

    Ndi zosangalatsa

    Kuona khamu lalikulu

    Likukulirabe

    Ndipo tonse tikuthandiza.

    Tonse tifuule

    Tiziitana anthu.

    ‘Bwerani kuphiri

    La Yehova Mulungu.’