Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 24

Bwelani ku Phili la Yehova

Bwelani ku Phili la Yehova

(Yesaya 2:2-4)

  1. 1. Taonani phili,

    Lokwezeka la M’lungu,

    Ilo ni phili la

    kulambila koona.

    Anthu ocokela,

    ku malo akutali.

    Abwela alambile

    Atate Yehova.

    Tsopano ocepa

    Akhala mtundu waukulu,

    Cifukwa Yehova

    amadalitsa nchito yathu.

    Anthu oculuka

    abwela kwa Yehova,

    Kuti acilikize

    Ucifumu wake.

  2. 2. Yesu, Mfumu yathu,

    Analamula kuti

    Ise tilalikile,

    uthenga wabwino.

    Iye aitana anthu,

    onse omvela.

    Kuti aphunzitsidwe

    mau a Yehova.

    Khamu lalikulu,

    onani mmene lakulila.

    Ndise okondwela

    kuti tili mu gulu ili.

    Tiyeni tiimbe,

    tiitanile ena

    Kuti nawo abwele,

    Ku phili la M’lungu.

(Onaninso Sal. 43:3; 99:9; Yes. 60:22; Mac. 16:5.)