NYIMBO 25
Chuma Chapadera
-
1. Odzozedwa ndi mtundu
Watsopano wa M’lungu.
Iye anawagula
Padziko lapansi.
(KOLASI)
Anthu odzozedwa
Ndi chuma chapadera.
Amakukondani.
Amalalikira za inu.
-
2. Ndi mtundu wapadera,
Wokonda choonadi.
M’lungu wawalandira
Mu kuwala kwake.
(KOLASI)
Anthu odzozedwa
Ndi chuma chapadera.
Amakukondani.
Amalalikira za inu.
-
3. Amasonkhanitsanso
Nkhosa zina mwakhama.
Ndi okhulupirika
Kwa Mwanawankhosa.
(KOLASI)
Anthu odzozedwa
Ndi chuma chapadera.
Amakukondani.
Amalalikira za inu.
(Onaninso Yes. 43:20b, 21; Mal. 3:17; Akol. 1:13.)