Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 26

Munacitila Ine

Munacitila Ine

(Mateyu 25:34-40)

  1. 1. Abale a Yesu

    ndi a nkhosa zina,

    Amatumikila mogwilizana.

    Zimene a nkhosa zina amacita

    Yesu Khristu adzazikumbukila.

    (KOLASI)

    “Munanitonthoza, poŵatonthoza.

    Zonse zimene munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.

    Zonse imwe munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.”

  2. 2. “Ninali na njala, ninali na njota,

    munabwela msanga munathandiza.”

    “Tiuzeni, izi

    tinacita liti?”

    Ndiyeno Mfumu idzayankha kuti:

    (KOLASI)

    “Munanitonthoza, poŵatonthoza.

    Zonse zimene munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.

    Zonse imwe munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.”

  3. 3. “Mokhulupilika munagwila nchito,

    yolalikila na abale anga.

    Landilani dziko

    na moyo wosatha.”

    Mfumu idzauza a nkhosa zina.

    (KOLASI)

    “Munanitonthoza, poŵatonthoza.

    Zonse zimene munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.

    Zonse imwe munaŵacitila,

    Imwe munali kucitila ine.”

(Onaninso Miy. 19:17; Mat. 10:40-42; 2 Tim. 1:16, 17.)