Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 27

Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera

Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera

(Aroma 8:19)

  1. 1. Posachedwa M’lungu wathu,

    Adzatisonyeza

    Kuti anthu odzozedwa

    Ndi ana akedi.

    (KOLASI)

    Khristu ndi odzozedwawo

    Adzapambanadi.

    Ulemerero wawonso

    Udzaonekera.

  2. 2. Omwe atsala padziko

    Adzaitanidwa.

    Khristu Mfumu ya mafumu

    Adzatenga onse.

    (KOLASI)

    Khristu ndi odzozedwawo

    Adzapambanadi.

    Ulemerero wawonso

    Udzaonekera.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Limodzi ndi Yesu Khristu

    Adzamenya nkhondo.

    Kenako ukwati wawo

    Udzachitikadi.

    (KOLASI)

    Khristu ndi odzozedwawo

    Adzapambanadi.

    Ulemerero wawonso

    Udzaonekera.