NYIMBO 29
Tizichita Zinthu Zogwirizana Ndi Dzina Lathu
-
1. Yehova Mulungu wamphamvuyonse,
Wachilungamo ndi wachikondi,
Mwini choonadi komanso nzeru,
Mukulamulira monga Mfumu.
Timasangalala potumikira
Ndi polengeza Ufumu wanu.
(KOLASI)
Tiyesetse kuchita zinthu zomwe
N’zogwirizana ndi dzina lathu.
-
2. Tikamatumikira ndi abale
Timakhaladi ogwirizana.
Tikaphunzitsa anthu choonadi,
Dzina lanu limatamandidwa.
Ndife odziwika ndi dzina lanu,
Tipitiriza kulitchukitsa.
(KOLASI)
Tiyesetse kuchita zinthu zomwe
N’zogwirizana ndi dzina lathu.
(Onaninso Deut. 32:4; Sal. 43:3; Dan. 2:20, 21.)