Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 30

Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa

(Aheberi 6:10)

  1. 1. Nthawi zina m’dzikoli,

    Moyo ungakhale wovuta.

    Koma ine nidziŵa

    Moyo ni wabwino.

    (KOLASI)

    Yehova ‘tate wanga, Adziŵa kuti nimukonda.

    Iye sadzanisiya; Ndipo sadzaniiŵala.

    Ngakhale nivutike Iye adzanisamalila.

    Yehova ni Bwenzi langa, M’lungu wanga.

  2. 2. Tsopano nakalamba;

    Nthawi ya mavuto yafika.

    Koma niyembekeza

    Dziko latsopano.

    (KOLASI)

    Yehova ‘tate wanga, Adziŵa kuti nimukonda.

    Iye sadzanisiya; Ndipo sadzaniiŵala.

    Ngakhale nivutike Iye adzanisamalila.

    Yehova ni Bwenzi langa, M’lungu wanga.

(Onaninso Sal. 71:17, 18.)