Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 32

Ima ku Mbali ya Yehova

Ima ku Mbali ya Yehova

(Ekisodo 32:26)

  1. 1. Panthawi ina ise tinali

    Mbali ya cipembedzo conama.

    Komabe, tinasangalaladi

    Kumvela za Ufumu.

    (KOLASI)

    Sankhani Yehova; mumtumikile.

    Sadzakusiyani; mvelani iye

    Ndipo lengezani Ufumu wake.

    Muŵauze onse Khristu ni Mfumu.

  2. 2. Tigwilizane, tilalikile

    Uthenga wabwino wa Ufumu.

    Nthawi yafika anthu asankhe

    Kutumikila M’lungu.

    (KOLASI)

    Sankhani Yehova; mumtumikile.

    Sadzakusiyani; mvelani iye

    Ndipo lengezani Ufumu wake.

    Muŵauze onse Khristu ni Mfumu.

  3. 3. Ise sitimayopa Satana,

    Timadalila Mulungu wathu.

    Ngakhale adani aculuke,

    M’lungu ni mphamvu yathu.

    (KOLASI)

    Sankhani Yehova; mumtumikile.

    Sadzakusiyani; mvelani iye

    Ndipo lengezani Ufumu wake.

    Muŵauze onse Khristu ni Mfumu.

(Onaninso Sal. 94:14; Miy. 3:5, 6; Aheb. 13:5.)