Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 33

Umutulire Yehova Nkhawa Zako

Umutulire Yehova Nkhawa Zako

(Salimo 55)

  1. 1. Chonde ndimveni Yehova

    musandinyalanyaze.

    Ndikuvutika mumtima

    chonde mundithandize.

    (KOLASI)

    Tulira Yehova nkhawa,

    Iye sangakusiye wekha.

    Akuteteza chifukwa ndi

    wokhulupirika.

  2. 2. N’kanakhala ndi mapiko

    ndikanaulukatu,

    Kuti ndibisale

    kwa ondichitira zoipa.

    (KOLASI)

    Tulira Yehova nkhawa,

    Iye sangakusiye wekha.

    Akuteteza chifukwa ndi

    wokhulupirika.

  3. 3. M’lungu akatitonthoza

    timapeza mtendere.

    Amatithandiza kuti

    tipirire mavuto.

    (KOLASI)

    Tulira Yehova nkhawa,

    Iye sangakusiye wekha.

    Akuteteza chifukwa ndi

    wokhulupirika.

(Onaninso Sal. 22:5; 31:​1-24.)