Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 34

N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

N’dzayenda mu Umphumphu Wanga

(Salimo 26)

  1. 1. Mlengi wanga, ine nikupempha

    Kuti mufufuze za mu mtima mwanga.

    Muniyese, O niweluzeni;

    Mudzapeza kuti nidalila imwe.

    (KOLASI)

    Koma ine, nikulonjezani

    Kuti nidzakhala wokhulupilika.

  2. 2. Sinikhala na anthu ocimwa,

    Nimapewa onse ocita zoipa.

    Conde m’saniononge pamodzi

    Ndi anthu ankhanza, ozonda co’nadi.

    (KOLASI)

    Koma ine, nikulonjezani

    Kuti nidzakhala wokhulupilika.

  3. 3. Nimakonda nyumba yanu M’lungu.

    Nimasangalala kulambila imwe.

    Nidzakulambilani mokondwa,

    Nidzaimba nyimbo zokutamandani.

    (KOLASI)

    Koma ine, nikulonjezani

    Kuti nidzakhala wokhulupilika.

(Onaninso Sal. 25:2.)