NYIMBO 38

Mulungu Adzakulimbitsa

Mulungu Adzakulimbitsa

(1 Petulo 5:10)

  1. 1. Panali chifukwa chimene Mulungu

    Anakupatsira choonadi.

    Anaona mtima wofuna kuchita

    Zabwino zomusangalatsadi.

    Unalonjeza kum’tumikira;

    Ndipo iye anakuthandiza.

    (KOLASI)

    Ndi magazi a Yesu

    Anakuwombola.

    Ndiwe wa Mulungu,

    adzakulimbitsa.

    Adzakutsogolera

    ndi mzimu woyera.

    Adzakulimbitsa

    adzakuteteza.

  2. 2. Mulungu anapereka Mwana wake;

    Amafunatu zikuyendere.

    Ngati Mwana wakeyo sanatimane

    Kukulimbitsa sangalephere.

    Chikondi chako sangaiwale;

    Sangasiye ndithu anthu ake.

    (KOLASI)

    Ndi magazi a Yesu

    Anakuwombola.

    Ndiwe wa Mulungu,

    adzakulimbitsa.

    Adzakutsogolera

    ndi mzimu woyera.

    Adzakulimbitsa

    adzakuteteza.