Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 39

Tipange Dzina Labwino na Mulungu

Tipange Dzina Labwino na Mulungu

(Mlaliki 7:1)

  1. 1. Timayesetsa tsiku lililonse,

    Kupanga dzina labwino na M’lungu.

    Tikapitiliza kumvela Yehova,

    Tikondweletsa mtima wake.

  2. 2. Kukondetsetsa zinthu za m’dzikoli,

    Kufunitsitsa kuti tilemele,

    Kulibe ubwino, tingasiye M’lungu.

    Sangatipatse madalitso.

  3. 3. Tifuna M’lungu atilembe dzina,

    Kuti tikhale mu buku la moyo.

    Lomba ndiye nthawi yakuti tipange

    Dzina labwino na Yehova.

(Onaninso Gen. 11:4; Miy. 22:1; Mal. 3:16; Chiv. 20:15.)