Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 43

Pemphelo la Mayamiko

Pemphelo la Mayamiko

(Salimo 95:2)

  1. 1. Yehova, Mulungu wamphamvuzonse,

    Tikufikilani mu pemphelo.

    Atate tagwada pamaso panu,

    Conde mvelani pemphelo lathu.

    Nthawi na nthawi ise timacimwa;

    Tipempha mutikhululukile.

    M’namutuma Yesu kudzatifela,

    Tifuna tikutumikileni.

  2. 2. Mulungu wathu tikuyamikila,

    Munatibweletsa m’gulu lanu.

    Tithandizeni, ‘se tiphunzitseni,

    Sitifuna kum’siyani imwe.

    Cifukwa ca mzimu wanu woyela

    Sitimayopa kulalikila.

    Mwacimwemwe tidzakutamandani,

    Ise tidzakutumikilani.

(Onaninso Sal. 65:2, 4, 11; Afil. 4:6.)