Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 45

Zimene Ndimaganizira Mozama

Zimene Ndimaganizira Mozama

(Salimo 19:14)

  1. 1. Zomwe ndimaganizira

    Mozama mumtima mwanga,

    Zizikusangalatsani

    Kuti ndikhale wolimba.

    Pamene ndili ndi nkhawa

    N’kumalephera kugona,

    Ndiganizire mozama

    Zinthu zondilimbikitsa.

  2. 2. Zilizonse zolungama,

    Zofunika ndi zoona,

    Ndikamaziganizira

    Zizindipatsa mtendere.

    Nzeru zanu n’zofunika

    Komanso ndi zochuluka,

    Choncho ndiziganizira

    Zonena zanu mozama.