Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 45

Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

Kusinkhasinkha kwa Mtima Wanga

(Salimo 19:14)

  1. 1. Zonse za mu mtima wanga,

    Zimene nimaganiza—

    Zikhale zokondweletsa

    Imwe Ambuye Yehova.

    Pamene nili na nkhawa,

    Na tulo osatuona,

    Nisinkhe-sinkhe za imwe

    Na pa zinthu zolungama.

  2. 2. Pa zilizonse zoyela,

    Na zilizonse zoona,

    Pa zonse zotamandika—

    Ine nidzaganizila.

    Maganizo anu M’lungu

    Amanipatsa mtendele.

    Ine niwasinkhe-sinkhe,

    Pa iwo niganizile.

(Onaninso Sal. 49:3; 63:6; 139:17, 23; Afil. 4:7, 8; 1 Tim. 4:15)