Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 51

Tinadzipeleka kwa Mulungu

Tinadzipeleka kwa Mulungu

(Mateyu 16:24)

  1. 1. M’lungu watikokela ise kwa Yesu.

    Afuna kuti tim’tsatile.

    Iye wationetsa

    Kuwala kwa co’nadi.

    Lomba ise tasankha

    Kutumikila Iye.

    (KOLASI)

    Tadzipeleka kwa Atate Yehova.

    Mwa iye na Yesu tikondwela.

  2. 2. M’pemphelo ise tilonjeza Yehova,

    Kukhala okhulupilika.

    Ise timakondwela

    Kulengeza za iye,

    Na za Ufumu wake,

    Ndipo sitidzaleka.

    (KOLASI)

    Tadzipeleka kwa Atate Yehova.

    Mwa iye na Yesu tikondwela.

(Onaninso Sal. 43:3; 107:22; Yoh. 6:44.)