Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 52

Tidzipeleke Monga Akhristu

Tidzipeleke Monga Akhristu

(Aheberi 10:7, 9)

  1. 1. Yehova Mulungu wathu

    Ni Mlengi wa zonse,

    Zakumwamba na pa dziko—

    Zinthu zonse n’zake.

    Anatipatsanso moyo

    Kuti ‘se tidziŵe

    Iye ni Mulungu woona,

    Tidzamutumikila.

  2. 2. Yesu anabatizika.

    Anadzipeleka

    Kutumikila Yehova,

    Mpaka imfa yake.

    Analonjeza Yehova,

    Monga wodzozedwa,

    Kuti adzamutumikila

    Na moyo wake wonse.

  3. 3. Yehova, Atate wathu,

    Ise tadzikana.

    Tadzipeleka kwa imwe,

    Ndise anthu anu.

    Munatuma Mwana wanu,

    Kuti atifele.

    Na mitima yoyamikila,

    Tidzalambila imwe.

(Onaninso Mat. 16:24; Maliko 8:34; Luka 9:23.)