Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 58

Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

Kufufuza Anthu Okonda Mtendere

(Luka 10:6)

  1. 1. Yesu anatilamula kuti

    Tiuze anthu uthenga,

    Amve mawu a Yehova.

    Ankakonda nkhosa za Mulungu.

    Ankazifufuza

    Mwakhama tsiku lonse.

    Nyumba ndi nyumba, mumsewu,

    Timauza aliyense

    Kuti posachedwa mavuto atha.

    (KOLASI)

    Tifufuze

    Okonda mtendere m’dzikoli.

    Tifufuze

    Ofuna kupulumutsidwa.

    Tifufuze

    Kulikonse.

  2. 2. Tifufuzebe anthu mwakhama.

    Alipo ambiri

    Omwe tingathe kuwathandiza.

    Poti timawakonda kwambiri,

    Tibwererekonso

    Tikawalimbikitse.

    M’matauni ndi m’midzinso,

    Tikapeza omvetsera

    Timasangalala powaphunzitsa.

    (KOLASI)

    Tifufuze

    Okonda mtendere m’dzikoli.

    Tifufuze

    Ofuna kupulumutsidwa.

    Tifufuze

    Kulikonse.