Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 59

Tamandani Yehova

Tamandani Yehova

(Salimo 146:2)

  1. 1. Titamande;

    M’lungu wathu.

    Amatipatsa zinthu zabwino.

    Tim’tamande,

    Tim’yamike.

    Iye amakonda anthu onse.

    Conco tilengeze dzina lake.

  2. 2. Titamande;

    M’lungu wathu.

    Amatiyankha tikapemphela.

    Dzanja lake;

    Ndi lamphamvu.

    Amalimbitsa anthu ofo’ka.

    Tilengeze kuti niwamphamvu.

  3. 3. Titamande;

    M’lungu wathu.

    Iye ni wolungama mu zonse.

    Adzakonza;

    Zolakwika.

    Anthu adzapeza madalitso

    Timutamande mosangalala.

(Onaninso Sal. 94:18, 19; 145:21; 147:1; 150:2; Mac. 17:25.)