Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 61

Pitani Patsogolo Mboninu

Pitani Patsogolo Mboninu

(Luka 16:16)

  1. 1. Olimba m’nthawi yamapeto ino

    Ndi atumiki olengeza uthenga.

    Mdyerekezi amawatsutsa,

    Ndi mphamvu za Yehova samagonja.

    (KOLASI)

    Ndiye pitani patsogolo mboninu.

    Sangalalani pogwira ntchito yake.

    Uzani onse zadziko latsopano

    Mmene mudzakhale madalitso.

  2. 2. Tisatengeke ndi moyo wofewa.

    Tizipewa kusangalatsa dzikoli.

    Tikane zochita za dziko

    Ndi kukhala okhulupirikabe.

    (KOLASI)

    Ndiye pitani patsogolo mboninu.

    Sangalalani pogwira ntchito yake.

    Uzani onse zadziko latsopano

    Mmene mudzakhale madalitso.

  3. 3. Ufumu wa M’lungu ukunyozedwa,

    Dzina lake loyera likudetsedwa.

    Tiyeni tiziliyeretsa.

    Tililengeze kumitundu yonse.

    (KOLASI)

    Ndiye pitani patsogolo mboninu.

    Sangalalani pogwira ntchito yake.

    Uzani onse zadziko latsopano

    Mmene mudzakhale madalitso.