Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 61

Patsogolo! Inu Mboni Zake

Patsogolo! Inu Mboni Zake

(Luka 16:16)

  1. 1. Mboni za Yehova n’zolimba mtima

    Zimalengeza Ufumu wa Yehova.

    Ngakhale Satana ‘zizunze,

    Sizileka, zidalila Yehova.

    (KOLASI)

    Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!

    Tumikilani Yehova na cimwemwe!

    Uzani onse kuti omvela M’lungu

    Adzakhala m’dziko latsopano.

  2. 2. Atumiki a Yehova Mulungu,

    Sacita mantha polalikila anthu.

    Samakonda zinthu za m’dziko;

    Iwo saiŵala Mulungu wao.

    (KOLASI)

    Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!

    Tumikilani Yehova na cimwemwe!

    Uzani onse kuti omvela M’lungu

    Adzakhala m’dziko latsopano.

  3. 3. Anthu amanyoza dzina la M’lungu.

    Samalemekeza ucifumu wake.

    Tiyeni’se tiwacenjeze;

    Tidziŵikitse dzina la Yehova.

    (KOLASI)

    Imwe Mboni za M’lungu, limbani mtima!

    Tumikilani Yehova na cimwemwe!

    Uzani onse kuti omvela M’lungu

    Adzakhala m’dziko latsopano.

(Onaninso Eks. 9:16; Afi. 1:7; 2 Ti. 2:3, 4; Yak. 1:27.)