Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 64

Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola

Timasangalala Kuthandizila pa Nchito Yokolola

(Mateyu 13:1-23)

  1. 1. Ino ni nthawi yokolola,

    Ni mwayi wosangalatsa.

    Onani mindayo yayela,

    Tiyeni ticite cangu.

    Yesu amatitsogolela,

    Pamene tilalikila.

    Timayamikila nchito iyi,

    Timaicita mokondwa.

  2. 2. Tigwile nchitoyi mwakhama,

    Pokonda anthu na M’lungu.

    Tiphunzitse onse mwam’sanga,

    Mapeto ayandikila.

    Cimwemwe cimene tipeza,

    N’dalitsodi la Yehova.

    Tigwile nchitoyi mosaleka,

    M’lungu adzatidalitsa.

(Onaninso Mat. 24:13; 1 Akor. 3:9; 2 Tim. 4:2.)