NYIMBO 66
Lengezani Uthenga Wabwino
-
1. Poyamba sitinkadziwa za Ufumu.
Pano tadziwa
Mfumu yolonjezedwa.
Mwa chifundo ndi chikondi cha Yehova
Anaganizira anthu ochimwafe.
Anakonza zoti pakhale Ufumu
Ndipo wolamulira waketu ndi Yesu.
Anakonzanso za kagulu ka nkhosa
Kodzakhala mkwatibwi wa Mwana wake.
-
2. Uthenga wabwinowu tisaubise,
M’lungu akufuna anthu audziwe.
Angelo amatithandiza kwambiri
Pogwira ntchito
yolengeza Ufumu.
Tapatsidwa udindo ndiponso mwayi
Wom’tamanda ndi kuyeretsa dzina lake.
Tikwaniritse udindo umenewu
Mwa kulalikira uthenga wabwino.
(Onaninso Maliko 4:11; Mac 5:31; 1 Akor. 2:1, 7.)