Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 66

Lengezani Uthenga Wabwino

Lengezani Uthenga Wabwino

(Chivumbulutso 14:6, 7)

  1. 1. Kale anthu sanadziŵe za Ufumu.

    Koma lomba na Mfumu yake tidziŵa.

    Mwa cifundo cake Atate Yehova,

    Anaganizila anthu ocimwafe.

    Anafuna Khristu adzalamulile;

    Panthawi yake,

    Ufumuwo unabadwa.

    Anasankha ena kudzalamulila

    Pamodzi na mwana wake Khristu Mfumu.

  2. 2. Cinali cifuno ca Yehova M’lungu.

    Kuti uthengawu ukalalikidwe.

    Angelo akondwa kutsagana nafe,

    Kutithandiza kulengeza Ufumu.

    Ni mwayi kukhala Mboni za Yehova.

    Kuyeletsa dzina lake

    na kum’tamanda.

    Timalemekeza nchito yathu iyi

    Yolengeza uthenga kwa anthu onse.

(Onaninso Maliko 4:11; Mac. 5:31; 1 Akor. 2:1, 7.)