Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 71

Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

(Aefeso 6:​11-​14)

  1. 1. Ndife gulu lankhondo

    La M’lungu wathu,

    Lotsogoleredwa ndi

    Mwana wake Yesu.

    Ngakhale titsutsidwe

    Sitimasiya,

    Sitiopa kanthu

    Ndife olimba.

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza

    Ufumu wayamba

    Kulamulira.

  2. 2. Ndife anthu a M’lungu.

    Tikufufuza

    Anthu omwe ndi nkhosa

    Zosowa za M’lungu

    Ndipo tikawapeza,

    Tiwaphunzitse,

    Tiwalimbikitse

    Tizisonkhana.

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza

    Ufumu wayamba

    Kulamulira.

  3. 3. Ndife gulu lankhondo

    Lomvera Yesu,

    Lokonzekera nkhondo

    Ndi lolimba mtima.

    Koma tikhale tcheru

    Kuti tisagwe,

    Zinthu zikavuta

    Tisafooke.

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza

    Ufumu wayamba

    Kulamulira.

(Onaninso Afil. 1:7; Filim. 2.)