Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 71

Ndife Asilikali a Yehova!

Ndife Asilikali a Yehova!

(Yoweli 2:7)

  1. 1. Ndife asilikali—

    Tilalikila.

    Olo Satana ‘tsutse

    Ise sitileka.

    Konse-konse tipita,

    Kukalalika.

    Timalimba mtima

    Sitimayopa.

    (KOLASI)

    Ndife asilikali—

    Timalengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulila.”

  2. 2. Ndife anthu a M’lungu—

    Tifunafuna

    Onse anasocela;

    Ni nkhosa za M’lungu.

    Ndipo tikaŵapeza

    Tiŵaphunzitse,

    Nakuŵaitana

    Kumisonkhano.

    (KOLASI)

    Ndife asilikali—

    Timalengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulila.”

  3. 3. Ise takonzekela

    Kumenya nkhondo,

    Yoteteza co’nadi

    Ku mitundu yonse.

    Tikhalebe olimba

    Kuti tisagwe.

    Zinthu zikavuta

    Ticilimike.

    (KOLASI)

    Ndife asilikali—

    Timalengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulila.”

(Onaninso Aef. 6:11, 14; Afil. 1:7; Fili. 2.)