NYIMBO 71

Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

Ndife Gulu Lankhondo la Yehova

(Yoweli 2:7)

  1. 1. Ndife gulu lankhondo,

    La M’lungu wathu.

    Lotsogoleredwa ndi

    Mwana wake Yesu.

    Satana angatsutse,

    Tilalikabe.

    Ndife osaopa

    Olimba mtima.

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulira.”

  2. 2. Ndife anthu a M’lungu,

    Ofunafuna,

    Anthu omwe ndi nkhosa,

    Zosowa za M’lungu.

    Tifuna kuwapeza,

    N’kuwaphunzitsa,

    N’kuwalimbikitsa:

    “Tizisonkhana.”

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulira.”

  3. 3. Ndife gulu lankhondo,

    Lomvera Yesu,

    Lokonzekera nkhondo,

    Lolimbatu mtima.

    Koma tikhale tcheru,

    Kuti tisagwe.

    Zinthu zikavuta,

    Tisafooke.

    (KOLASI)

    Ndife gulu lankhondo.

    Tikulengeza:

    “Ufumu wayamba

    Kulamulira.”