Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 72

Tikulalikira Choonadi Chonena za Ufumu

Tikulalikira Choonadi Chonena za Ufumu

(Machitidwe 20:​20, 21)

  1. 1. Poyamba sitinkadziwa

    Zinthu zoti tizichita.

    M’lungu anatipatsa

    Choonadi ndi kuwala

    Ndipo tinazindikira

    Chifuniro cha Yehova,

    Kuti tim’tumikire

    Ndi kumalengeza dzina lake.

    Timalalikira anthu

    Mumakomo ndi mumsewu.

    Timathandiza anzathu

    Kuti adziwe Yehova.

    Tiyeni tiziyesetsa

    Kulalikira mwakhama

    Mpaka pomwe Yehova

    Adzanene kuti tamaliza.