NYIMBO 75

“Ine Ndilipo! Nditumizeni!”

“Ine Ndilipo! Nditumizeni!”

(Yesaya 6:8)

  1. 1. Lero anthu akunyoza

    Dzina loyera la M’lungu.

    Ena amati n’ngwankhanza.

    Enanso: “Kulibe M’lungu.”

    Ndani adzaliyeretsa,

    Dzina la Yehova M’lungu?

    (KOLASI 1)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni!

    Ndidzaimbira inuyo.

    Ndi mwayi waukulu, Mbuye.

    Ine! Nditumizeni!’

  2. 2. Anthu osaopa M’lungu;

    Akumati akuchedwa.

    Amalambira mafano,

    Ena eti Kaisara.

    Ndani adzawachenjeza

    Za nkhondo ya M’lungu wathu?

    (KOLASI 2)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni!

    N’dzachenjeza mosaopa.

    Ndi mwayi waukulu, Mbuye.

    Ine! Nditumizeni!’

  3. 3. Anthu ofatsa ’kulira

    Zoipa zikuchuluka.

    Iwo amafunitsitsa

    Choonadi chomasula.

    Ndani adzawatonthoza?

    Ndani adzawathandiza?

    (KOLASI 3)

    ‘Ndilipo! Nditumizeni!

    Ndidzaphunzitsa ofatsa.

    Ndi mwayi waukulu, Mbuye.

    Ine! Nditumizeni!’