Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 78

Kuphunzitsa Mawu a Mulungu

Kuphunzitsa Mawu a Mulungu

(Machitidwe 18:11)

  1. 1. Tikamaphunzitsa anthu

    Timasangalala.

    Timapeza madalitso

    Ochuluka ndithu.

    Timatsanziratu Yesu

    Pophunzitsa ena

    Ndiponso timawathandiza

    Kukonda Mulungu.

  2. 2. Pamene tikuphunzitsa

    Tichite zabwino,

    Anthu onse aziona

    Kuwala kwa M’lungu.

    Timafufuza mwakhama

    Mawu a Mulungu.

    Pouza ena uthengawu

    Timadziphunzitsa.

  3. 3. M’lungu watipatsa zoti

    Tiziphunzitsira

    Ndipo tikamamupempha

    Adzatithandiza.

    Timakonda mawu ake

    Omwe ndi oona.

    Tizikonda anthu omwe

    Timawaphunzitsawo.