Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 84

Kudzipeleka na Mtima Wonse

Kudzipeleka na Mtima Wonse

(Mateyu 9:37,38)

  1. 1. Yehova amatipatsa

    Zinthu zotisangalatsa.

    Afuna tisangalale

    Pamene titumikila.

    (KOLASI)

    Mokondwa tifuna,

    kudzipeleka.

    Ndipo kulikonse,

    tipita mofunitsitsa.

  2. 2. Kuno tili kuli nchito,

    Yofunika kuigwila.

    Tionetsa khama lathu,

    Pothandiza anthu onse.

    (KOLASI)

    Mokondwa tifuna,

    kudzipeleka.

    Ndipo kulikonse,

    tipita mofunitsitsa.

  3. 3. Kulikonse kuli anthu,

    Na ku malo akutali.

    Tipita kukalengeza

    Uthenga kwa anthu onse.

    (KOLASI)

    Mokondwa tifuna,

    kudzipeleka.

    Ndipo kulikonse,

    tipita mofunitsitsa.

(Onaninso Yoh. 4:35; Mac. 2:8; Aroma. 10:14.)