Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 86

Tiziphunzitsidwa

Tiziphunzitsidwa

(Yesaya 50:4; 54:13)

  1. 1. Bwerani mosangalala muphunzire.

    “Bwerani mumwe madzi a moyo.”

    Nonse anjala bwerani mudye

    Ndi kudzalandira malangizo.

  2. 2. Tisasiyetu kusonkhana pamodzi.

    Tiziphunzitsidwa ndi Mulungu.

    Kuno n’kumene kuli abale,

    Kuno kuli mzimu wa Mulungu.

  3. 3. Lilime lophunzitsidwa choonadi

    Limasangalatsa kulimvera.

    Tisonkhane ndi anthu a M’lungu.

    Tizipezeka pamisonkhano.