Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 87

Bwerani Mudzalimbikitsidwe

Bwerani Mudzalimbikitsidwe

(Aheberi 10:​24, 25)

  1. 1. Tili mu dziko lomwe ndi loipa,

    Anthu sakudziwa M’lungu.

    Choncho tikufunika malangizo

    Oti atitsogolere.

    Misonkhano yathu imathandiza

    Kukhala osangalala.

    Timamvako mawu olimbikitsa

    Cholinga tisafooke.

    Sitidzasiya kugwiritsa ntchito

    Malamulo a Yehova.

    Pamisonkhano timalangizidwa

    Kumakonda choonadi.

  2. 2. Yehova amadziwa bwino zinthu

    Zomwe timafunikira.

    Tikamasonkhana timasonyeza

    Kuti timamudalira.

    Malangizo ochoka kwa akulu

    Amakhala othandiza.

    Timadziwa kuti sitili tokha

    Abale amathandiza.

    Choncho poyembekezera m’tsogolo

    Tisasiye kusonkhana.

    Tiziphunzira kugwiritsa ntchito

    Mawu a Mulungu wathu.