Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 87

Bwelani Mutsitsimulidwe!

Bwelani Mutsitsimulidwe!

(Aheberi 10: 24, 25)

  1. 1. Tili m’dziko la anthu osocela

    Iwo sadziŵa co’nadi.

    Kuti ’se tipewe njila zoipa,

    Tifunika citsogozo.

    Misonkhano imatitsitsimula,

    Imatilimbikitsadi.

    Itithandiza kukhulupilila

    Mwa Yehova M’lungu wathu.

    Conco ise sitidzataya konse

    Malamulo a Yehova.

    Misonkhano imatiphunzitsadi

    Kukondabe coonadi.

  2. 2. Yehova M’lungu ni Atate wathu;

    Timvele uphungu wake.

    Tidzipatula nthawi yosonkhana

    Kuti tikhale anzelu.

    Polabadila akulu mu mpingo

    Ise ticita zabwino.

    Monga banja la m’cikhulupililo

    Mpingo umatithandiza.

    Conco pamene tiyembekezela

    Tsogolo lathu lowala,

    Tidzapitilizabe kuphunzila

    Nzelu zocoka kumwamba.

(Onaninso Sal. 37:18; 140:1; Miy. 18:1; Aef. 5:16; Yak. 3:17.)