NYIMBO 87

Bwerani Mudzasangalale

Bwerani Mudzasangalale

(Aheberi 10:24, 25)

  1. 1. Tikukhala m’dziko lomwe n’loipa;

    Anthu sakudziwa M’lungu.

    Choncho tifunikatu malangizo,

    Oti atitsogolere.

    Misonkhano yathu imathandiza;

    Kukhala osangalala.

    Timamvako mawu olimbikitsa

    Cholinga tisafooke.

    Sitidzasiya kugwiritsa ntchito;

    Malamulo a Yehova.

    Pamisonkhano timalangizidwa;

    Kukondatu choonadi.

  2. 2. Yehova amadziwa bwino zinthu;

    Zomwe tikufunikira.

    Tikamasonkhana timasonyeza

    Kuti timamudalira.

    Malangizo ochoka kwa akulu,

    Amatithandiza zedi.

    Timadziwa kuti sitili tokha,

    Iwo adzatithandiza.

    Choncho poyembekezera m’tsogolo,

    Tisasiye kusonkhana.

    Tiziphunzira kugwiritsa ntchito

    Nzeru yochoka kumwamba.