Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 88

Ndiphunzitseni Njira Zanu

Ndiphunzitseni Njira Zanu

(Salimo 25:4)

  1. 1. Yehova tasonkhanatu pamodzi

    Pomvera kuitana kwanu.

    Mawu anu ndi nyale m’njira yathu,

    Amatiphunzitsa za inu.

    (KOLASI)

    Ndiphunzitseni njira zanuzo,

    Ndikhale womvera malamulo.

    Ndiyendetseni m’njira yoona,

    Ndizikonda malamulo anu.

  2. 2. Nzeru zanu Yehova ndi zozama.

    Mfundo zanu n’zolimbikitsa.

    Mawu anu adzakhala kosatha,

    Timapezamo zodabwitsa.

    (KOLASI)

    Ndiphunzitseni njira zanuzo,

    Ndikhale womvera malamulo.

    Ndiyendetseni m’njira yoona,

    Ndizikonda malamulo anu.