NYIMBO 90
Tizilimbikitsana
-
1. Pomwe tikulimbikitsana
Kutumikira Yehova,
Chikondi chathu chimakula
Ndipo timagwirizana.
Chikondi cha anthu a M’lungu
N’chothandiza kupirira.
Timatetezedwa kwambiri
Tikamakhala mumpingo.
-
2. Mawu a pa nthawi yabwino
Amatilimbikitsadi.
Mawu otilimbikitsawa
Amachoka kwa abale.
Kugwirira ntchito limodzi
Kumatigwirizanitsa.
Tizikhala olimbikitsa
Ndipo tizithandizana.
-
3. Pamene tsiku la Yehova
Layandikira kwambiri,
Tipitirize kusonkhana
Kuti tiyende ndi M’lungu.
Tigwirizane ndi abale,
Titumikire limodzi.
Choncho tizilimbikitsana
Kuti tikhulupirike.
(Onaninso Luka 22:32; Mac. 14:21, 22; Agal. 6:2; 1 Ates. 5:14.)