Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 90

Tilimbikitsane Wina na Mnzake

Tilimbikitsane Wina na Mnzake

(Aheberi 10:24, 25)

  1. 1. Pamene tilimbikitsana

    Kutumikila Yehova.

    Cikondi cathu cimakula;

    Timapezadi cimwemwe.

    Cikondi timaonetsana,

    Cimatilimbikitsadi.

    Mpingo ni pothaŵila pathu,

    Ni malo a citetezo.

  2. 2. Mwa mau athu acikondi

    Timatonthozadi ena.

    Ndipo timaŵalimbikitsa

    Kuti iwo asafo’ke.

    Kumatipatsadi cimwemwe

    Kuseŵenzela pamodzi.

    Conco tizilimbikitsana

    Ndipo tizithandizana.

  3. 3. Tsiku la Atate Yehova,

    Tidziŵa layandikadi.

    Tifunika tizisonkhana

    Kuti tikapulumuke.

    Tiyeni tizithandizana

    Kusunga umphumphu wathu.

    Monga banja logwilizana

    Tidzalimbikitsanadi.

(Onaninso Luka 22:32; Mac. 14: 21, 22; Agal. 6:2; 1 Ates. 5:14.)