Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 91

Ntchito Yomwe Tagwira Chifukwa cha Chikondi

Ntchito Yomwe Tagwira Chifukwa cha Chikondi

(Salimo 127:1)

  1. 1. Yehova tikufuna

    Kupemphera mothokoza

    Chifukwa mwatikonda

    Potipatsa nyumbayi.

    Taona mwadalitsa

    Ntchito imene tagwira

    Ndipo taimanga chifukwa

    Mwatithandiza.

    (KOLASI)

    Kukumangirani nyumbayi

    Yehova unali mwayi.

    Tilemekeze dzina lanu nthawi zonse

    Ndi kukutumikirani.

  2. 2. Ndife osangalala

    Kuti tapeza anzathu.

    Sitidzaiwala mpakana

    M’Paradaiso.

    Taona mzimu wanu

    Chifukwa chogwirizana.

    Uwu unali mwayi wokweza

    Dzina lanu.

    (KOLASI)

    Kukumangirani nyumbayi

    Yehova unali mwayi.

    Tilemekeze dzina lanu nthawi zonse

    Ndi kukutumikirani.