Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 94

Tiyamikila Mau a Mulungu

Tiyamikila Mau a Mulungu

(Afilipi 2:16)

  1. 1. Tikuyamikani Atate wathu,

    Cifukwa mwatipatsa Mau anu.

    Amatitsogolela atipatsa nzelu.

    Coonadi cake catimasula.

  2. 2. Mau anu M’lungu, ali na mphamvu.

    Akhudza zolinga za mtima wathu.

    Mfundo zanu, Yehova, zitipatsa nzelu.

    Zititsogolela m’zocita zathu.

  3. 3. Mau anu M’lungu, atithandiza.

    Kuphunzila kwa aneneli anu.

    Conde tithandizeni tikhale olimba.

    Tikuyamikani Mulungu wathu.

(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)